Lyrics

Anandikonda munthene ndisanabadwe Amkayimba tinyimbo mwanawe utonthole Anali pompa nsanayimilire Anandikwawitsa anandiphuzitsa kuyenda Nkhope yanu sindingayiwale Ngayiwale ngayiwale nono Ntchito zanu ndiwulure Ndiwulure ndiwulure (lure) Amayi anga sindingawanyoze Ndili moyo sangamavutike Kachala kanga sindingawatoze Malipiro sindingawamalize Amayi anga sindingawasale Kuchepa komko tikanyemelane Cha m'ma four phee tilangizane Malipiro sindingawamalize Musadabwe khalidwe ndinabela ma ine Kuyankhula maonekedwe kaoneni ma ine Musadabwe thanzilo Ndili ndi mdalitso Palowapo thandizo, zosezo zigwere Ma ine, Ma ine Ndisaname timamvana ndisaname timamva! Ma ine, Ma ine Tidzayimba jabulani tidzayimba jabula! Nzoyamwira kuti ukhale mfumu mkoyambira Ooh nanji ndidwale ndipomwe muwadiwire Ooh oh maso awo Ukawaona muli njira zawo Muli masophenya mwana wawo Kuti zitheke nditengepo gawo Ooh ndipo zithuzi zawo Atandifungatira m'manja mwawo Zimawulura za mkati mwawo Muli chikondi mtimwa mwawo Musadabwe khalidwe ndinabela ma ine Kuyankhula maonekedwe kaoneni ma ine Musadabwe thanzilo Ndili ndi mdalitso Palowapo thandizo, zosezo zigwere Ma ine, Ma ine Ndisaname timamvana ndisaname timamva! Ma ine, Ma ine Tidzayimba jabulani tidzayimba jabula! Ma ine, Ma ine Ndisaname timamvana ndisaname timamva! Ma ine, Ma ine Tidzayimba jabulani tidzayimba jabulaaa! Njuchi
Lyrics powered by www.musixmatch.com
instagramSharePathic_arrow_out