Lyrics

Ine ndikhumba, Mbuye Yesu Mudzakhale pompo mkamadzafa Ndikamasimba za imfa yanga Abwenzi ambiri samakondwa Koma ndithu tonsefe tidzafa Ngati si mawa mwina mkuja Ine nditi pa maliro anga Msadzachulutse kundiyamika Nzimu wanga udzakondwa, (powona kuti) Odwala athandizidwa (mwachangu ndi chikondi) Pa anthenda aweluzidwa (asanamangidwe) Wana amayi amasiye (zawo alandire) Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito Abale anga osawuka-wa mukawaganizira Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Musadzagule bokosi lodula Musadzatchule zakutchuka kwanga Musadzanene za chuma changa Musadzanene za nzeru zanga Ngati mudzafune kunena kanthu Mudzati ndidayesetsa kumenya Kumenya nkhondo yabwino Ndinali soldier kwa amphawi Nzimu wanga udzakondwa, (powona kuti) Odwala athandizidwa (mwachangu ndi chikondi) Pa anthenda aweluzidwa (asanamangidwe) Wana amayi amasiye (zawo alandire) Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito Abale anga osawuka-wa mukawaganizira Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Aah ooh Abwenzi anga sanali achuma Anali olema ndi amphawi Andende olira mdzipatala Iih amayi amasiye Musadzayiwale ndinayesetsa Kukonda mtundu wa munthu Mtembo wanga msawutaye ntchire Ana a mawa adzakumbuke Nzimu wanga udzakondwa, (powona kuti) Odwala athandizidwa (mwachangu ndi chikondi) Pa anthenda aweluzidwa (asanamangidwe) Wana amayi amasiye (zawo alandire) Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito Abale anga osawuka-wa mukawaganizira Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wangawu udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito Abale anga osawuka-wa mukawaganizira Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Soldier udzagona Nzimu wa Marley udzagona Nzimu wa Toshi udzagona Nzimu wa Etsi udzagona Nzimu wa Luther udzagona Nzimu wa Ghandi udzagona Nzimu wa Chirwa udzagona (Nzimu wa Yesu udzagona)
Lyrics powered by www.musixmatch.com
instagramSharePathic_arrow_out