Lyrics

Bisa bisa bisa bisa bisa Udzawulure zikadzatheka Tiuze mungokhala chete bisa Adzangowona zikadzayenda Pakuti dziko linayipa Ladzadza afisi ndi mibulu ya jealous Udzingosunga mu mtima mwako Adzingodziwa Mbuye yekha, wakumwamba Uzingokomela anzako Koma usamangomvera zilizonse Si onse ukucheza nawo amakukonda Abwenzi lero mawa adani Samangokhulupira onse Yemweyo ukudya nayeyo adzakupeleke Kaya ufuna kugula nyumba Adzangowona ukadzagula Ngati ufuna kugula galimoto Adzangowona ukuwa waver Kaya wapeza wako Ufuna kumanga banja Adzangowonera pa wedding card Usamalengeze zinthu zilizonse Umampatsa mpata Satana Zimkayenda bwino kale Pomwe amkadya kachetechete Samkapitapita kumudzi Moyo wake udali wamphamvu Ana kubala apite kumudzi Wakaputa mavu pachisa Chonsecho adawatengera katundu wankhaninkhani Adawatengeranso ndalama Bisa bisa bisa bisa bisa Udzawulure zikadzatheka Tiuze mungokhala chete bisa Adzangowona zikadzayenda Pakuti dziko linayipa Ladzadza afisi ndi mibulu ya jealous Udzingosunga mu mtima mwako Adzingodziwa Mbuye yekha, wakumwamba Uzingokomela anzako Koma usamangomvera zilizonse Si onse ukucheza nawo amakukonda Abwenzi lero mawa adani Samangokhulupira onse Yemweyo ukudya nayeyo adzakupeleke Chinali chibwenzi chobeba Amkangocheza mwachinsisi Adamuchemelera pagulu Kuti bwezi lake ndi wachuma Sanadziwe kuti anzake amkasilira Zinthu zayamba kuvuta Lero sakuyankha phone Sakuyankha message Mwapeleka momwetamweta Bisa bisa bisa bisa bisa Udzawulure zikadzatheka Tiuze mungokhala chete bisa Adzangowona zikadzayenda Pakuti dziko linayipa Ladzadza afisi ndi mibulu ya jealous Udzingosunga mu mtima mwako Adzingodziwa Mbuye yekha, wakumwamba Uzingokomela anzako Koma usamangomvera zilizonse Si onse ukucheza nawo amakukonda Abwenzi lero mawa adani Samangokhulupira onse Yemweyo ukudya nayeyo adzakupeleke
Lyrics powered by www.musixmatch.com
instagramSharePathic_arrow_out