Lyrics

Moyo uno anthu Inu ndi ovuta Pali zokoma pamakhala zowawa Yamika yemwe agonjetsa zowawa Mudzasangalala Moyo uno uli ngati uchi Pali uchi pamakhalanso njuchi Kuyamika yemwe mwadziotcha njuchizo Udzadya malesa Mukamawalangiza anawa Musamawabisire zambiri Poti mwadzidzidzi mwina Inu mudzafa Adzalira! Mukamawalangiza anawa Musamangowauza adzakhala bwana Poti mwinamwakwe adzakhala antchito Adzalira! Mukamamulangiza mwanayo Mumuwuze m'moyo muli mavuto ndi zokoma Bread tidye lero mawa chinangwa Ndiye moyowo! Moyo wa munthu pali nthawi yokondwa Komanso dziwa kuti pali nthawi yolira Ngati sunavutike ukali wang'ono Thokoza Mulungu Mukamawalangiza anawa Musamawabisire zambiri Poti mwadzidzidzi anzaga mudzafa Adzalira! Mukamawalangiza anawa Musamangowauza adzatola ndalama Poti mwinamwakwe adzataya ndalama Adzalira! Musamale pofuna kuthandiza Pokuti nzukwa umaoneka monga nzimu Si onse omwe udzawathandize adzasangalare Ambuye anati kondani adaniwo Omwe achenjera poti satana ndi mdaniso Mukapusa mudzayanjana ndi satana Mu dzina la Mbuye Mukamawalangiza anawa Musamawabisire zambiri Poti mwinamwake anzanga tidzafa Adzalira! Mukamawalangiza anawa Musamangowauza adzakhala a police Poti mwinamwakwe adzakhala akayidi Adzalira! Mukamawalangiza anawa Musamawabisire zambiri Poti mwadzidzidzi mwina Inu mudzafa Adzalira! Mukamawalangiza anawa (Musamangowauza adzakhala a ndalama) (Poti mwinamwakwe adzataya ndalama) (Adzalira!)
Lyrics powered by www.musixmatch.com
instagramSharePathic_arrow_out