Lyrics

Oh oh oh oh Oh no no, oh no no Oh ooh Mukati mutchene ma label bwana Perfume ndi hugo boss Galimoto ya mtundu wa hummer Nyumba yanu ngati reserve bank Mkazi aliyese amasilira Olo atakhala mkazi wachitatu, chilichose azizipangira Bola azitchedwa akazi anu Koma chomwe chidabwitsa Kusiya ulemelero wonsewo Kubwela kuno kwa Che Musa Kuzandilanda wangayu Oh ooh ooh, no Ndisiyireni kanga Ndi komwe ndili nako ine Ndikomwe mbuye anandipatsa Ndisiyireni bwana Ine ndilibe hummer, ngakhale tv ndilibe ine Mwa iyeyo ndipeza zonse Ndisiyireni bwana Usakhale ngati mfumu David Inali ndi chuma chambirimbiri Kubwela mlendo, kupanda chifundo Kukapha ka nkhosa ka mphawiyo Muli ndi chuma chambirimbiri Ma lorry, ma bus ndi zigayo Ife timkadyero wokala yomweyo Mwazamangapo grocery Koma chomwe chidabwitsa Kusiya chuma chonsecho Kubwela kuno kwa Mayaka Kudzaphangira amphawi Oh ooh ooh Ndisiyireni kanga Ndi komwe ndili nako ine Ndikomwe mbuye anandipatsa Ndisiyireni bwana Ine ndilibe hummer, ngakhale tv ndilibe ine Mwa iyeyo ndipeza zonse Ndisiyireni bwana Ndisiyireni kanga Ndi komwe ndili nako ine Ndikomwe mbuye anandipatsa Ndisiyireni bwana Ine ndilibe hummer, ngakhale tv ndilibe ine Mwa iyeyo ndipeza zonse Ndisiyireni bwana Iwe mkazi wanga usatengeke Gwero la chuma chawo sukulidziwa Mwina ndi zakuba, zophera anthu Uzangosandutsidwako ndondocha Ali ndi ngongole zambirimbiri Kuti agone amamwa barium Amaoneka wolemera kunjaku Mumtima mwawo mulitu umphawi Timadya bonongwe mosangalala Osati nkhuku zawo za tcheu tcheu Mtendere wamumtima uposa zose Nthawi yathuso izafika Bwera mkazi wanga tsono tivine Tinyadire, tithokoze Mulungu Ali ndi cholinga pokutilenga Ona ma bwana akukusilira Mwamuna uja mudataya Lero ndi phungu wachuma Chikhwaya chija mutsata Chidalowa pagalaputi Oh ooh ooh, no oh Ndisiyireni kanga, (ayi ayi ayi ayi) Ndi komwe ndili nako ine, (oh oh oh) Ndikomwe mbuye anandipatsa, (oh oh oh) Ndisiyireni bwana Hummer ndilibe ine, ine ndilibe hummer Tv ndilibe ine,ngakhale tv ndilibe ine, (ooh oh) Mwa iyeyo ndipeza zonse. (ooh oh) Ndisiyireni bwana Ndisiyireni, ndisiyireni kanga Ndisiyireni, ndi komwe ndili nako ine, (oh oh oh) Ndikomwe mbuye anandipatsa, (oh oh oh) Ndisiyireni bwana Hummer ndilibe ine, ine ndilibe hummer Tv ndilibe ine,ngakhale tv ndilibe ine, (ooh oh) Mwa iyeyo ndipeza zonse. (ooh oh) Ndisiyireni bwana
Lyrics powered by www.musixmatch.com
instagramSharePathic_arrow_out