Lyrics

Abambo anawasiya amayi ndili wang'ono Ana asanu ndi awiri amayi okha Amayi opanda ntchito, osaphunzira Kuwalanda katundu yense, opanda chifundo Mudasankha uchidakwa, kusiya wana Tidasanduka masikini abambo mulipo Kuvundukula ma bin, kutolatola chakudya Kupita ku misika, tikatole za magwafa Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Pamene tidali kukula, anatitola azungu Kutilipilira sukulu, kutigwiritsa maganyu Tinkakolopa mchimbuzi, opanda nsapato kuphanzi Kuvutikira sukulu, abambo mukumwa mowa Adayesetsa amayi, mpaka lero ndakula Nditangoyamba ine ntchito, amayi kumamwalira Ukwati wanga amayi, sanawuwone Mwana ndi nkazi wanga, amayi anawazemba ooh! Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Ndithokoza kwa Ambuye, kamba kankazi wanga Andisamala mwachikondi, ngati mayi wanga Mundandilanda amayi, mwandipatsa Roller Abambo anachoka, mwandipatsa Jonny ooh Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Chabwino mayi Zembani Mupume mumtendere Kumwamba muli amayi Mukonze malo anga Mama we love you This song is specially dedicated to you mom It's been three years since you lay down there But we will still remember you Your are a hero mama You are a hero mama
Lyrics powered by www.musixmatch.com
Get up to 2 months free of Apple Music
instagramSharePathic_arrow_out