Lyrics

Kodi wanyonga ndiye uti Osakumana ndi mikwingwirima Njira yomwe onse amoyo Ayesedwa kulimba mtima Zochititsa mantha ena Zilimbitsa mtima ena Tifanana ndikusiyana muzotipangitsa kulira Timalira mu mtima Mong'ung'udza ndi modandaula Ululu ukasefukira timaliraso mwa mkuwe Kulira kulibe mulingo Champweteka ndiye ayamba Sikuona nkhope kulira mayi maso ndiye mboni Tose timalira Zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo) Timalira zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo) Timalira mumtima timalira monga ana Ndimisozi nayo imakhala ikulakatika Timalira mumtima Mayo Nthawi zina ndimalira Ndikakumbuka zowawa zimene ndaziona ine m'moyo Moyo ndichonchobe basi Mtima ulinayo misozi Yoseoneka yongothera mkati Ndimisozi yosapuputika amayo!! Ooh ooh ooh Ooh weh tsamba langa Kuwala mudzuwa gwelera mumphepo Kukongola kwako kosiliritsa kuli kunja Ulira mkati Oooh weh tsamba langa Lira mumphepo asazindikire Dziko likonda wolimba mtima mwana wanga Tose timalira Zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo) Timalira zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo) Timalira mumtima timalira monga ana Ndimisozi nayo imakhala ikulakatika Timalira mumtima
Lyrics powered by www.musixmatch.com
instagramSharePathic_arrow_out